Malingana ndi kukwera kwa mitengo ya feteleza m’dziko muno, bungwe la Centre for Environmental Policy and Advocacy (CEPA) lalimbikitsa alimi kugwiritsa ntchito manyowa omwe amathandizilanso kubwezeletsa chonde mu nthaka.
Project Coordinator wa bungweri, Tamala mataka wamema alimiwa lachisanu pomwe amayendela ntchito yopanga manyowa a compost m’mudzi mwa chimamba mfumu yaikulu Njewa mu mzinda wa Lilongwe.
Mataka wati pomwe mitengo ya feteleza ikunka nakwelera – kwelera, ndi bwino kuti alimi atengepo gawo pogwiritsa ntchito manyowa omwe ndi otsikilako mtengo poyelekeza ndi feteleza yemwe amagugitsa nthaka.
“ife cholinga chathu tufuna kulimbikitsa alimi kugwiritsa ntchito manyowa mu minda mwawo zomwe zithandizile kubwezeletsa chonde mu nthaka kuti alimi azitha kukolola zakumunda zochuluka”, anatelo Mataka.
Iye anati ntchito yopanga manyowa anthu anayilandila kwambiri ndipo alimi ali kalikiliki kupanga manyowa kut akathile kuminda kwawo pomwe ena akumagulitsa kuti apeze kangachepe.
Poyankhulapo, Mkulu Oyang’anila ntchito yopanga manyowa ku gulu la Gospel to All, Korrinto Saddom mu mudzimo wati ntchito yopanga manyowa ikuyenda bwino ndipo ikuthandiza kubwezeletsa chonde mu nthaka.
“Chiyambileni ntchitoyi mu mudzi muno, alimi takhala tikuthira manyowa – wa ku minda kwathu ndipo ena timagulitsa kuti tipeze ndalama zomwe zikumatithandizila moyo wathu wa tsiku ndi tsiku”, anatelo Saddon.
Bungwe la CEPA lidayamba ntchito yopanga manyowa mu November Chaka cha 2022 ndipo ntchitoyi ikuyembekeza kutha mu November 2025. Bungweli lakhala likugwira ntchitoyi mu mizinda iwiri ya Blantyre komanso Lilongwe.