Bungwe loyendetsa masewero a mpira wamiyendo mdziko muno la Football Association of Malawi (FAM), lero lalengeza kuti lathetsa mgwirizano wake ndi mphunzitsi wa timu yaikulu yadziko lino, Patrick Mabedi.
Malingana ndi uthenga wapatsamba lamchezo la FAM, Mabedi wachotsedwa kamba kakusachita bwino kwa timu ya dziko lino.
“Komiti yowona za aphunzitsi ku FAM itakumana yagwirizana zochotsa Mabedi kamba kakusachita bwino kwa timu komaso kulephela kwa timuyi kudzigulira malo mu mpikisano wa AFCON omwe uchitike 2025” unatero uthengawu.
Timu yadziko linoyi yelephera kutolela poyinti olo imodzi mu gulu L momwe iyi itaseweramo masewero anayi odzigulira malo ku AFCON.
Koma FAM yati ikhale ikulengeza mayina a aphunzitsi omwe apitilize ntchitoyi mogwilizira asanalembe ena okhanzikika.
Kuchoka pomwe anakhala mphunzitsi wogwirizira wa Flames, Malawi yasewera masewero 17.
Timuyi inapambana kasanu komaso kufananitsa mphamvu katatu.
Masewero omwe inagonja ndi asanu ndi anayi (9). Koma mwa masewero amenewa pali awiri omwe inagonja mmapenate ku COSAFA kutsatila kufananitsa mphamvu.
Kuchotsedwa kwa Mabedi ngati mphunzitsi wa timu ya dziko lino, kwakhala kwachikhumi pazaka khumi ndi chimodzi (11) zapitazi.
Mu February 2013, Malawi inachotsa ntchito Kinnah Phiri yemwe anayitengela Flames ku AFCON ya 2010 ndipo mmalo mwake munalowa Eddington Ng’onamo.
Koma chaka chomwecho mu Julaye, FAM inalemba ntchito mphunzitsi waku Belgiam Thom Santifiet.
Uyu sanalimbeso kamba koti anachotsedwa chaka chotsatila mu 2014 ndipo mmalo mwake munalowa Young Chimodzi Snr.
Kuchoka apo, panangothaso chaka chimodzi pomwe FAM inalemba ntchito Enerst Mtawali mu 2015 yemwe anafika mpaka 2017 pomwe anachotsedwaso ndipo kunabwera mphunzitsi waku Belgiam Ronny Van Geneugden mmalo mwake.
Zinthu zinankerankera ziyipila kotero kuti FAM inachotsa RVG mu 2019 ñdikulemba Meke Mwase ngati ongogwilizira.
Nayeso Mwase ntchito yake sinalimbe ndipo anawonetsedwa nsana wa njira mu 2021 ndipo FAM inalemba ntchito Mario Marinica waku Romania.
A Marinica zawo zinada kumayambiliro kwa 2023 pomwe FAM inalemba ntchito Mabedi mu April mpaka pano pomwe amuchotsa ntchito.
I do agree with all the ideas you have introduced on your post They are very convincing and will definitely work Still the posts are very short for newbies May just you please prolong them a little from subsequent time Thank you for the post