Komiti yoyendetsa masewero a Nkhonya mchigawo chapakati ya Central Region Boxing Committee (CRBC) yati ikusaka ndalama yokwana 2 Million Kwacha yothandizila Nkhonya yomwe akonza kumathero kwa Julaye.
Mlembi wamkulu wakomitiyi Alex Henry Sakala wati mwambowu udzachitika pa 8 Julaye 2024 ku Grand Business Park mu mzinda wa Lilongwe komweso kudzachitikile nkhonyayi.
Sakala wati zomwe akonza pa 8 Julaye, zizathandiza kugula zipangizo zosewelera Nkhonya.
“Takonza zochitika zosiyanasiyana ku Grand Business Park lolemba pa 8 July 2024. Mwambowu udzachitika ngati njira yodzapezela ndalama zokwana 2 Million Kwacha yomwe idzathandize pa Nkhonya yomwe tidzakhale nayo Julaye yomweyo pa 27 ku Grand Business komweko”
“Pa 8 Julaye lomwe nditsiku lofuna kupeza ndalamayi takonza majowajowa, Nkhonya yansangulutso, zothamangathamanga za ana komaso zina zambiri”
“Tikadzayipeza ndalama tikufunayi idzatithandiza kugula zovala mmanja ndi kuphazi zawosewela athu komaso zopangila zokonzekera pamasewelo a Nkhonya” anatero Sakala.
Iye anapitiliza kupempha akufuna kwabwino kuti athandizile ganizoli kuti zokhumba za komitiyi zizakwanitsidwe.
Grand Business Park imapezeka ku mseu wa Bypass mu mzinda wa Lilongwe.