Mphunzitsi wa Silver Strikers Peter Mponda wati cholichonse sichimatheka masana atsiku la lero pomwe atuluka mu FDH Bank Cup atagonja kwa Blue Eagles.
Ma timu awiriwa analephelana posagoletsana chigoli ndipo ma penate ndiwomwe anaweluza zonse pa bwalo la Nankhaka.
Mecium Mhone, Jacob Robert, Lanken Mwale, Andrew Juvinala komaso Ganizani James anamwetsa onse asanu a Blue Eagles.
Ma Banker anagoletsa kudzela mwa Chimwemwe Idana, Maxwell Paipi komaso Nickson Mwase pomwe Innocent Shema analephela kugoletsa penate yake kuti masewelo athele 5 kwa 3 kupambana Blue Eagles.
Koma poyankhula atatha masewerowa, mphuzitsi wamkulu wa Silver Strikers Peter Mponda anavomeleza kuti mpira unawakanika mtsiku la lero.
“Cholichonse lelori sichimatheka, kusunga mpira, kupanga mwayi wazigoli, ngakhale kumenyela pagolo panalibe chigawo chonse choyamba”
Mponda watiso akukhulupila kuti kugonja kwawo kwadza kamba koti osewela ake amaphweketsa timu ya Blue Eagles yomwe ikusewela ligi yaying’ono ya Chipiku.
Kumbali yake mphunzitsi wa Blue Eagles Elia Kananji wati anauza anyamata ake kuti abweze chipongwe chomwe Silver Strikers inawapanga chaka chatha pomwe inawatulutsa muchikho chomwechi.
“Mukumbukira bwino Silver Strikers inatitulutsa mu quarter final chaka chatha ndiye ndinauza anyamata anga kuti nthawi yobweza yakwana”.
Kananji wati chisinsi chaosewela ake pakadali pano ndichoti akusewela mopsa mtima ndikutuluka kwawo mu Super League chaka chatha.
Zateremu Blue Eagles yafika mundime yamatimu 16 mu mpikisano wa FDH wachaka chino.
Hi i think that i saw you visited my web site thus i came to Return the favore Im attempting to find things to enhance my siteI suppose its ok to use a few of your ideas