Katswiri wa team ya Mallumo Gallants mdziko la South Africa, Frank Gabadinho Mhango wasiyidwa pa mndandanda wa osewela a team ya Malawi.
Flames ikuliwela ku Senegal komwe ikasewere ndi timu ya dzikolo lachisanu likubwelali ndipo ma team awiriwa adzakumanaso pa 15 October kuno kumudzi.
Ngakhale Football Association of Malawi inapempha Mphunzitsi wadziko lino Patrick Mabedi kuti atenge Gaba ndi osewela ena akunja kwa dziko lino, izi sizinatheke kamba koti pandandandawu palibepo katswiriyu.
Mabedi watenga koyamba otseka kumbuyo chakumamzere wa Mighty Mukuru Wanderers Timothy Silwimba, pomwe akatswiri awiri omwe amasewera ku Mozambique Lloyd Njaliwa komaso Richard Mbulu abwelera mu team yadziko lino atasowa kwa kanthawi.
Wina yemwe wabwelela mu timuyi ndi otchinga pagolo wa Blue Eagles Brighton Munthali yemwe sanapezeke masewero omwe Flames inasewela ndi Burkina Faso komanso Burundi mu September kamba kovulala.
Nawu ndandanda wa osewela omwe Patrick Mabedi watenga:
Pagolo: George Chikooka (Silver Strikers) and Brighton Munthali (Blue Eagles)
Kumbuyo: Mark Lameck, Nickson Mwase (Silver Strikers), Stanley Sanudi, Lawrence Chaziya, Timothy Silwimba (Mighty Mukuru Wanderers), Chembezi Denis (Al Qasim SC-Iraq)
Pakati: Liyod Aaron(FCB Nyasa Big Bullets), Wisdom Mpinganjira (Mighty Mukuru Wanderers), Chimwemwe Idana (Silver Strikers), Lanjesi Nkhoma, Patrick Mwaungulu (TP Mazembe-DRC), John Banda (UD Songo-Mozambique), Yamikani Chester, Lloyd Njeliwa (Costa do sol-Mozambique), Robert Saizi (Zanaco-Zambia)
Kutsogolo: Zeliat Nkhoma (Kamuzu Barracks), Chawanangwa Kaonga (Zanaco-Zambia), Richard Mbulu ((Costa do sol-Mozambique)