Chipatala chachikulu cha Ntchisi chapempha kampani zomwe sizaboma kuti zithandize kuthetsa mavuto omwe chikukumana nawo.
Mkulu wa ntchito zoyan’gangira madotolo m’boma la Ntchisi, Dr Yakobe Machira, ndiye wamemeza kampanizi Lachisanu pachitalachi polandira katundu wapafupifupi K13 miliyoni kuchochera ku bungwe la Central Medical Stores Trust (CMST).
Machira wati kaamba koti chipatala cha Ntchisi chili ndi udindo waukulu woyang’anira odwala, yomwe ndi ntchito yolira ndalama zambiri, thandizo loyendetsera chipatalachi lochoka ku Boma pena silikwanira kufikira zofuna zonse.
Apa Machira anati kampani zomwe zili zomasuka zithandize ndi mayendedwe odalirika, kukonza zipinda za ogwira ntchito komanso zosungiramo odwala, ngakhalenso kugula mankhwala ndi zipangizo zothandizira odwala.
Mwa zomwe kampani ya CMST yapereka pali zofunda, matilesi komanso zipangizo zothandizira ntchito za uchembere wabwino.
M’busa Gamaliel Kalebe yemwe ndi m’modzi mwa akuluakulu a komiti yoonetsetsa kuti ntchito za kampani ya CMST zikuyenda m’chimake anati komitiyi idayendera chipatalachi mwezi wa Meyi, pomwenso idazindikira kuti pali zingapo zomwe CMST ingachite mwachangu pothandiza chipatalachi.
Iye adati ndizoona kuti thandizo lochokera ku boma limagwira kale ntchito yayikulu yomwe kuti iyende bwino imasowekeranso thandizo kuchoka kwa onse omasuka kuthandizapo.
Kalebe adati pempho lachipatalachi komanso thandizo la CMST zili monga mwa chiphunzitso cha Malembo Oyera pa Mateyu 25 omwe amati omwe athandiza ena achita izi mokomera chiphunzitso chaMulungu.
























