Oyimba odziwika bwino, Stella Kantwanje Chimtolo yemwe amadziwika ndidzina loti “Blessed Stella” wati zokonzekera mwambo wachikondwelero choti wakwanitsa zaka 21 akuyimba zikupita kumalecheleche.
Katswiri oyimba nyimbo zauzimuyu wati wayitana woyimba osiyanasiyana pamwambowu, omwe udzachitike pa 6 July 2024 ku Chill Sport, m’boma la Mchinji.
“Zokonzekera zikuyenda bwino ndipo zikupita kumapeto kuti ku Chill Sport kukhale chikondwelelo choti ndakwanitsa zaka 21 ndikutumikira ambuye kudzera mmayimbidwe”
“Zaka 21 simasewera, ndadutsa muzambiri zomwe zikanatha kundibwezera m’mbuyo koma Mulungu wandipyoletsa mpaka pano”.
Malingana ndi Blessed Stella, oyimba ngati Kamuzu Barracks Gospel Singers, Favoured Martha, Phalyce Mang’anda, Violet Tengani Dumba, Farai Chazima, Bertha Nkhoma ndi ena ochuluka, adzakhala akuyimba patsikuli kuyambila 1 koloko masana.
Iye anapitiliza kumema anthu kudzafika ndikukondwela ndimayimbidwe osiyanasiyana patsikuli.
“Oyimba oposa 30 pamtengo wa K2500 akulu komaso K1500 ana, zikungoonetselatu kuti tangofuna kuwapatsa chikondwelelo anthu aku Mchinji komaso madela ozungulira”
Chiyambile kuyimba, Blessed Stella watulutsa ma abamu anayi.
Muma abamu ake atatu oyimbilira omwe ndikuphatikiza “Tagwiranji” komaso “Ndi Wabwino Yesu”, katswiriyu amadziwika ndidzina loti Stella Kantwanje koma wasintha dzina pomwe akutchuka ndidzina loti Blessed Stella mu abamu yake yatsopano momwe muli nyimbo yomwe yatchuka yotchedwa “Jericho”.
Thank you for your sharing. I am worried that I lack creative ideas. It is your article that makes me full of hope. Thank you. But, I have a question, can you help me?