Mmodzi mwa anthu amene akupikisana nawo pa mpando wa mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), Alex Major wati kusowa kwa dzina lake pa mndandanda wa anthu ovomelezeka kutenga nawo mbali pa mpikisanowu ndizinthu zazing’ono kusiyana ndizimene wadutsamo.
Poyankhula pamsonkhano wa olemba nkhani mumzinda wa Lilongwe, Major wati ngakhale dzina lake silinatchulidwe lachiwiri pomwe utsogoleri woyendetsa chisankhochi umalengeza mndandanda wa omwe ayimile, koma iyeyo ayimila nawo pazisankhozi.
“Oyendetsa masankho MCP sapanga chiganizo chomaliza koma National Executive Committee (NEC) osati zomwe zikuvekazi ndiye ine pa 8 pano ndiyimila nawo ndipo ndikhala pa pepala la mavoti.
“Zomwe zikuchitika padakali panozi kumamva kuti ena akumenya nkhondo yoletsa amzawo kuyimila ndizazing’ono, ife tatulutsilanapo zikwanje ku MCP koma nkhani yabwino ndiyoti zonse zimatha ndikukambilana monga chipani chamtendere,” Iwo anatelo
Iye wati zomwe zachitikazi zikudza kamba koti anthu asanu ndi awiri (7) mwa omwe amapanga mndandandawu akuyimila nawo pa zisankhozi.
Major analangizaso anthu ovota kuti akasankhe anthu omwe alibe mbiri ya katangale komanso wolemekeza mfundo zamigwirizano yomwe imachitika mchipani.
Mwa anthu 224 omwe anawonetsa chidwi chofuna kuyimila nawo pa chisankhochi, 20 sakupezeka kuphatikiza yemwe amafuna kuyimila pa udindo wa wachiwiri kwamtsogoleri wachipanichi Vitumbiko Mumba.
I have been surfing online more than 3 hours today yet I never found any interesting article like yours It is pretty worth enough for me In my opinion if all web owners and bloggers made good content as you did the web will be much more useful than ever before
I don’t think the title of your article matches the content lol. Just kidding, mainly because I had some doubts after reading the article. https://accounts.binance.com/en/register?ref=JHQQKNKN