By Lusako Ng’ambi:
Lipoti la komiti ya nyumba yamalamulo yoona za chisamaliro cha anthu la m’zaka za 2020/2021 lasonyeza kuti ndende pafupifupi 27 m’dziko muno zikukumana ndi vuto la njala.
Izi zadziwka pomwe wapampando wa komitiyi a Savel Kafwafwa amapereka zomwe anapeza potsatira kafukufuku yemwe komitiyi inachita komanso zokambirana pa ndende ya Zomba, pomwe anati akayidi amakhala masiku atatu osadya chakudya.
Lipotili lasonyeza kuti nthawi zina akayidi ankadya nsima yopanda ndiwo, kapena phala lopanda mchere ngakhale shuga.
A Kafwafwa anati vutoli linadza kaamba ka ndalama zachakudya zomwe ndendezi zinapatsidwa zinathera panjira chifukwa cha kukwera mtengo wa chimanga.
Iwo ati chuma chomwe boma linaapeleka ku ndendezi sichinagwirizane ndi mmene Iwowo anaganizira kaamba ka kukwera mtengo wa zinthu.
Iwo ati ngati komiti, akupempha boma kuti lisinthe lamulo lomwe ndendezi zimagwiritsa ntchito la 1955 ndicholinga choti ndendezi ziziziimira pazokha kaamba koti pakadali pano lamuloli silikuwalola kutelo.
Akafwafwa apemphaso boma kuti lipange komiti yapadera kapena libweretse pamodzi ma komiti osiyasiyana kuti apeze njira zoonetsetsa kut ndende mziko muno zikuzidalira pazokha.
Komabe aphungu enaa sanagwirizane ndi ganizo lomathandiza akayidi powapatsa ndalama, ponena kuti munthu sungathandize munthu yemwe ali mu ndende atha kuchita zaumbanda.