Ndendende dzaka 12 zapita pomwe Silver Strikers inamang’ala ku Football Association of Malawi (FAM) kamba koti Complex Madrid yomwe inawagonjetsa inaseweletsa katswiri yemwe ankati sanali oyenela.
Mu 2012, Complex Madrid yomwe inali akatswiri a m’boma la Zomba inagonjetsa Silver Strikers 2-1 mu Presidential Cup.
Koma Silver Strikers inamang’ala ku FAM kuti Madrid inagwiritsa ntchito Aicco Maluwa yemwe ankati anali atasewera kale ku timu ina mundime yachipulula m’boma la Zomba asanalowele ku Madrid.
Izi zinapangitsa FAM kulamula kuti Silver Strikers ipitilile mu mpikisanowu.
Dzanadzanali Ma Banker afaso mu mpikisano wa Castel ndi timu yosewera League yaying’ono ya Leyman Panthers zigoli zinayi kwazitatu pamapenate, mphindi 90 zitathera 2-2.
Ngakhale Silver Strikers yatuluka mu mpikisanowu, koma pali mwayi oti itha kupitilira pomwe yakamang’alaso ku FAM ponena kuti Panthers inagwiritsa ntchito osewera awiri osaloledwa.
Malingana ndizomwe tapeza, Silver Strikers yadandaula kuti Taniel Mhango anatumikira kale Ekwendeni United pomwe Aggrey Msowoya anasewelera Mhuju mumpikisanowu, asanasewele ndi Silver Strikers mu ndime yamatimu 32.
Ndipo pakadali pano FAM kudzera mwa Gomezgani Zakazaka yati yalandira dandaulo ndipo ikufufuza za nkhaniyi.