Wapampando wa bungwe la anthu a ulumali mu mzinda wa Lilongwe, la Lilongwe City Disability Citizen Forum (LCDCF), a Gerald Nankhwende apempha boma kuti lipatule unduna wa anthu awulumali kuti ukhale pawokha.
A Nankhwende ayankhula izi lachiwiri pomwe Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (NICE) pamodzi ndi bungwe lowona za alumali la FEDOMA amakumana ndi nthumwi za bungwe la LCDCF.
Iwo anati kuphatikizana kwa unduwu kuti adziyang’anila anthu awulumali, achikulile komaso kuwona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi, zimalepheletsa anthu awulumali kupeza thandizo loyenela ku undunawu.
“Panafunika pakhale nduna yongoyang’anila za ulumali pawokha kusiyana ndipano pomwe nduna imodzi imayang’anila zawulumali, achikulile ndikuti pasakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi”.
“Panopa timatha kupita kukafuna thandizo ku unduna koma kuti tithandizidwe zimakhala zovuta kamba koti pena timapeza ofesi ikupanga za anthu achikulile kapena zakusasiyana kwa amuna ndi akazi, izi zimalepheletsa kuthandizidwa nkhawa zathu” anatero Nankhwende
A Nankhwende anawululaso kuti anthu amaulumali akukumana ndi nkhaza zosiyanasiyana ndipo anapempha adindo kuwaganizila.
“Tikusalidwa, zamtukuka pakhomo, ngongole za NEEF sitikupatsidwa nawo”
“Komaso zikukhala zovuta anthu awulumali kugwilitsa ntchito malo ena aboma ngati mmasukulu komaso mzipatala kamba koti mulibe zipangizo zotiyeneleza”
Ndipo mmau ake Charles Banda yemwe ndiwapampando oyang’anila anthu amaulumali mumzinda wa Lilongwe ku Bungwe la FEDOMA wati ngakhale boma likuyesetsa kuti thandizo lake lifikile aliyese, koma adindo a mmadela ndiomwe akumasala anthu awulumali.
Banda anapitiliza kulonjeza kuti FEDOMA ipitilizabe kuthandiza bungwe la LCDCF komaso mabungwe ena kuti anthu amaulumali apeze thandizo lofunika.
Mkulu okoza zochitika-chitika kubungwe la NICE mumzinda wa Lilongwe, Hajira Ali anati mkumano omwe unachitika lero ndiumodzi mwamikumano yomwe bungwe la NICE likuchititsa ndi mabungwe osiyasiyana.
Ali anati mkumanowu wathandiza kudziwitsa anthu amaulumali ufulu wawo komaso kuwalimbikitsa kuti adzitenga nawo mbali pazinthu zosiyanasiyana zokhudza miyoyo yawo yatsiku nditsiku.