Mphunzitsi wa FOMO FC Gilbert Chirwa wati akulimba mtima kuti timu yake singatulule mu TNM Super League ngakhale zinthu zisakuyenda pakadali pano.
FOMO inalowa mu Super League chaka chino itatenga ukatswiri mu League yachigawo chakumwera.
Pomwe yamaliza masewero a chigawo choyamba cha League ya chaka chino, FOMO FC yapambana kanayi, kufananitsa mphavu katatu ndipo yagonja kasanu ndikatatu (8).
Izi zikutanthauza kuti timu yaku Mulanjeyi ili ndimapoint khumi ndi asanu (15) ndipo ili pa number 13.
Poyankhula atatha masewero omwe FOMO yachitaya yokha ndikulephelana ndi Mighty Tigers 2-2, Gilbert Chirwa wati ngakhale timu yake ili kumusi koma situlula mu League yi.
“Ngati coach ndikuwakhulupira anyamata anga, tikhalabe mu League” anatero Gilbert Chirwa.
Ngati njira yofuna kudzipulumutsa mu League yi, Chirwa wati akhale akubweletsa osewela ena msika ogula ndikugulitsa ukatsekulidwa kuti alimbitse timuyi.
Mmasewero a lerowa FOMO FC inatsogola mchigawo choyamba kudzela mwa Hassan Hussein komaso Hassan Lwembe koma Tigers inabweza mchigawo chachiwiri kudzera mwa Daniel Shadreck ndi Precious Chipungu.
Thank you for your sharing. I am worried that I lack creative ideas. It is your article that makes me full of hope. Thank you. But, I have a question, can you help me?