Phungu wa nyumba ya malamulo wa dela la Dedza Mayani, Savel Kafwafwa wapempha anthu a derali kuti amuikenso pa m’pando pomuvotela pa 16 september pano ndicholinga choti apitilize ntchito ya zitukuko zomwe akupanga kuderali.
Kafwafwa yemwe anali phungu wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) wati aima pa yekha (Independent) pa zisankho zikubwelazi.
Kafwafwa wanena izi lachisanu pa Chitundu Primary School Ground mu boma la Dedza komwe bungwe la National Initiative for Civic Education – NICE linakonza mtsutso wa anthu onse omwe akuzapikisana nao pa mipando ya makansala komanso aphungu.
Kafwafwa wati afuna kukwanilitsa masomphenya ake omanga nseu wa tala omwe uli kale mundondomeko ya zachuma ya dziko lino komanso akufuna kuonetsetsa kuti amange chipatala chachikulu mu derali popeza anthu amayenda pafupifupi makilomita 55 kupita kuchipatala chachikulu cha Dedza.
Poonjezela, Kafwafwa anati afuna kulimbikitsa ulimi osadalira Mvura kwenikweni malingana ndi Kusintha kwa nyengo ndicholinga choti athetse vuto la njala lomwe lakhudza derali.
Iye wati zitukuko zonsezi kuti zitheke, ali okonzeka kugwira ntchito limodzi ndi chipani chilichonse chomwe chilowe m’boma pa zisankho zikubwelazi.
“m’maganizo anga zitukuko monga nseu wa tala, chipatala chachikulu, zikuyenela a boma- akumtundawo kuti avomeleze ndipo nthawi zina ngati sukugwira nao bwino ntchito amatha kukumana zinthu ngati zimenezi. Nde palinso Ubwino okhalira mu boma”, anatelo Kafwafwa.
Poyankhula ndi mmodzi yemwe anatenga nawo mbali pa mtsutsowu yemwe akupikisana nao pa m’pando wa ukansala ku Chitundu Ward, a Chikondi moses wa chipani cha DPP wati afuna kuzaimila ku derali kaamba koti amayi ambiri amapondelezedwa ndipo iye afuna azatukule miyoyo yao akamuika pa udindo .
Poyankhulanso ndi a Mfumu a derali omwe amaimila mfumu yaikulu Tambala ayamikila bungwe la NICE pokodza mtsutsowu ndipo awapempha kuti apitilize kupeleka maphunziro ndi upangili kwa anthu kuti kaundula oponya voti azakhale wa bata ndi mtendele.
“Ife tikuthokoza kwambiri a nice potiunikila kuti chisankho si nkhondo ndipo aliyense amene azapambane kaya ndi phungu, kaya ndi kansala azagwire ntchito limodzi popanda mavuto alionse”, a Tambala anatelo.























