Katswiri wosewela pakati Peter Banda wabwelera ku timu yake yakale FCB Nyasa Big Bullets pamgwirizano wazaka zitatu.
Katswiri wazaka 24-yu, wabwelera ku Bullets komwe anachokako chaka chatha pomwe anakhalako miyezi inayi ndikuthandiza timuyi kutenga zikho zinayi.
Banda anasewera masewero ake omaliza asanachoke ku Bullets mu ndime yotsiliza ya Airtel Top 8 pomwe timuyi inagonjetsa MAFCO FC pa 6 January.
Poyankhula atasaina mgwirizanowu Peter analonjeza wochemelera Bullets kuti ayembekezele zintchito zopambana kuchoka kwa iye.
“Ndikungoyamika Mulungu pondipatsaso mwayi wachiwiri. Ndikuyamikaso utsogoleri wa Bullets, maninjala wanga komaso banja lakwathu pondipatsa chilimbikitso. Uwu ndimwayi watsopano ndipo sindiyankhula zambiri, koma ndikangochila ndikulonjeza kuti anthu adzawona Peter wosinthika” anatero Banda.
Ndipo mmau ake mkulu woyang’anila zintchito za FCB Nyasa Big Bullets Albert Chigoga anati ndiwokondwa kubweleraso kwa Peter Banda.
Chigoga watsimikizaso kuti timuyi ikhale ikumuthandiza Peter Banda kuti achile.
“Sizoona kuyang’anila mwana wachichepele ngati uyu kuti angotha motere kamba kovulara. Ali ndizaka 24 zokha taganiza zotengapo gawo chifukwa akufunika thandizo lathu”
“Tili ndichikhulipiro kuti akalandila thandizo lake ku Kenya, adzakhala mbali imodzi ya timu yathu mu chaka cha 2025” anatero Chigoga.
Peter Banda wasewerapo ma timu a Sheriff Tiraspol ku Moldova, Simba SC yaku Tanzania komaso posachedwapa anapeza mwayi wopita ku Red Arrows yaku Zambia koma zinakanika kamba koti ndiwovulala.