Kunali chiphokoso kuti wooooo! Pa Kamuzu Stadium mu mphindi 71 zamasewero apakati pa FCB Nyasa Big Bullets komanso Bangwe All Stars mu TNM Super League.
Panja pa bwaloli ena amvekele ‘Maulle-tu amenewo ayikamo’, potengela kuti apa ndipomwe amalangila matimu. Koma sizinali chomcho kamba koti anali mnyamata ochenjera kwambiri, Clever Chikwata yemwe anamwetsa pagolo la Maulle.
Pompo-pompo, osewela a Maulle kuchita timikumano, nkumafusana kuti chitedze apalamula anawa titani kuti chiwayabwe.
Timu ya wanthuyi inayesetsa kuponya mizinga koma checheche, yankho osapezeka mpaka Bullets kufera pakhomo ngati chigayo.
Pomwe amagoletsa Chikwata inali Bullets itataya mipata yambirimbiri komaso kukhala kwambiri ndimpira kuyambira gawo loyamba.
“Timakhala ndimpira malo osafunika, sitimaponya kwambiri golo lawo komaso tikuchinyitsa kwambiri nthawi yomwe tapanikiza” -anatero mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets, Kalisto Pasuwa.
Atafusidwa ngati pali mwai otenga ukatswiriwu, mphunzitsi waku Zimbabweyu anati amenyabe nkhondo mpaka kumaliza masewero onse omwe atsala nawo.
Ngakhale yapambana Bangwe ikanali kuchigwa cha imfa ndimapoints 15 pamasewero 20 omwe yasewela.
“Ndinawauza osewela anga kuti sitili pabwino, tikalimbikile kuti tizipatse mwayi wovuuka mu chigwachi” anatero Travor Kajawa, mphunzitsi wa Bangwe All Stars.
Mphunzitsi yemwe wabwela kumene ku Bangweyu wati kupambana kwa lero ndichiyambi chazinthu zabwino ku Bangwe ndipo akulimba mtima kuti apulumuka mu ligiyi.
Apa ndie kuti mbiri zatsopano zalembedwa zingapo.
Clever Chikwata wakhala osewela oyamba wa Bangwe All Stars kumwetsa pagolo la FCB Nyasa Big Bullets.
Aka kanali kachisanu pakati pamatimuwa mmipikisano yonse ndipo Bullets inali itapambana kanayi konse, osachinyitsa komaso kuchinya zigoli 10.
Kuchoka 2015, aka ndikoyamba Maulle kugonja katatu pamasewero 17 a ligi. Ndipo kuchoka 2017 timuyi yalephelaso koyamba kufika ma points 30 pamasewero 17 pomwe pano yangotolela 24 okha, nkumasuyana ndi Silver Strikers yomwe ikutsogola ndimapoints ndimapoints 21.
Apa ndie kuti Maulle kukhale kovuta kuteteza ukatswiri wa Super League chaka chino kamba koti yatsakama pa 10, pandandanda wamatimu mu ligiyi.