Bungwe la WaterAid lati kuchepekela kwa ndalama ku nthambi yoona za madzi ndi ukhondo kukusokomeza kwambiri ntchito yothana ndi matenda monga kolera m’dziko muno.
Izi zadziwika kaamba Ka zotsatila za kafukufuku yemwe bungweli lidachita
M’modzi mwa ogwira ntchito ku bungweri Chandilira Chisi wati Chaka ndi Chaka ndalama yokwana 200 million Us Dollars ndiyomwe imafunikila kuti aliyense afikilidwe ndi madzi a ukhondo mdziko muno koma Pakadali pano 100 million Us Dollars ndiyomwe imagwiritsidwa ntchito zomwe zikupeleka chiopsezo chothana ndi matenda okhudza madzi ndi ukhondo monga kolera.
Chisi wapempha boma komanso Nthambi zonse zokhuzidwa kuti akhale ndi chidwi choika ndalama zochuluka ku Nthambi yoona za madzi ndi ukhondo ndicholinga chofuna kuthana ndi matenda omwe amadza kaamba Ka mavuto amadzi opanda ukhondo.
“ngati dziko tigwirizane tiikemo ndalama zochuluka kwambiri ku nkhani ya madzi ndi ukhondo chifukwa mavuto amene angathe ndi ochuluka kwambiri “, Chisi natelo.
Pothililapo ndemanga, m’modzi mwa akuluakulu ogwira ntchito ku wabungwe la zakafukufuku la Institute for Policy Research and Social Empowerement, Joseph Thombozi wati pa mbali pobweretsa ndalama zambiri ku Nthambi yoona za madzi ndi ukhondo, iye wati ngati liyambe lasamalilira kaye ndalama zomwe zilipozi kuti zizigwira ntchito yake yoyenelela.
“Pasakukwanitsa kupezeka ndalama zimenezi palinso zina zomwe zikutaika mkati momo kudzera mukuononga, katangale komanso kusasamala chuma ngati dziko choncho, tikuyenela kusamalila kaye ndalama zilipozi”, Thombozi anatelo.