Komiti yoyang’ana kayendetsedwe ka chuma mnyumba ya malamulo yati makampani ambiri aboma alipachowopsezo chotsekedwa.
Wapampando wa komitiyi Mark Bottoman waulula izi munyumba yamalamulo lero pomwe amapeleka lipoti la momwe ma kampaniwa akugwilira ntchito.
Malingana ndi lipotili, makampani ambiri sakutsatila malamulo oyendetsela chuma chaboma.
“Mukumbukila kuti tili ndimalamulo ambiri wothandizila pakuyendetsa chuma cha boma mmakampanimo, Koma tawona kuti molingana ndi lipoti yomwe tapelekayi, ambiri sakutsatila”
“Chinthu china ndichoti makampani ambiri aboma makamaka ESCOM komaso Water Board, akulephela kutenga ngongole ku nthambi zosiyanasiyana zaboma komaso kuma unduna omwe sakulipila madzi komaso magetsi. Komaso makampaniwa akhala akutenga ngongole zambiri zimene akulephela kuzibweza. Ngongolezi zikulephetsa magwilidwe awo antchito” anatero Bottoman
Bottoman anapitiliza kuchenjeza kuti ngati boma silisamala, makampani ambiri atsekedwa zomwe ziyike pachipsinjo a Malawi ambiri potengela kuti amadalira makampaniwa.
Choncho, Bottoman anapempha mlembi wamkulu wa ofesi ya mtsogoleri wadziko lino kuwayitanitsa adindo mmakampaniwa ndikuwunikila bwinobwino lipoti lapelekedwali ndimmene angakonzere zinthu zawo.