Kunali chisangalalo pamudzi wa Mwanang’ombe kwa Mfumu yayikulu Phambala ku Ntcheu pomwe amene akufuna kudzaimira mpando wa phungu wa kunyumba ya malamulo mchipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) kudera la kum’mwera m’bomali Engineer Joe Ching’ani amapereka nyumba yophunzitsiramo ana maphunziro a mmera mpoyamba.
Engeneer Ching’ani wati nyumbayi yomwe wamanga ndi ndalama pafupipafupi 7 Million kwacha, ikuyembekezeka kutukula ntchito za maphunziro komanso kakhonzedwe ka ana pa mayeso aboma ponena kuti iye amakhulupilira kuti mmera mpoyamba ndipo nkhani ya maphunziro ikulimbikitsudwa ndi mtsogoleri wadzikolino Lazarus Chakwera mu masomphenya a dziko a Malawi 2063.
“Maphunziro ndi maziko a tsogolo labwino ladera ndipo kuti dera kuti likhale lotukuka pamasoweka maphunziro abwino kwa achinyamata. Tawona mbuyomu achinyamata athu kuno ku Ntcheu asakuchita bwino ndipo ndi zodziwikiratu kuti gwera la izi ana athu sitikuwapatsa maphunziro ali achichepere, nchifukwa chake mafumu kuno atandipempha sindinazengereze koma kumanga nyumba iyi yomwe itukule ntchito zamaphunziro kwathu kuno,” adatero Ching’ani.
Poyankhula atalandira mphatsoyi, Inkosi Phambala idati ndiyokondwa kuti munthu amene akufuna kudzakhala mtsogoleri akuika patsogolo ntchito za maphunziro ndipo izi zikuonetsa kuti Engineer Ching’ani ali ndi masomphenya abwino a derali.
Pa mfundoyi, Inkosi Phambala yapempha makolo kuderali kuti alimbikitse ana aang’ono kupita ku sukulu yamkaka komanso atenge udindo osamalira nyumbayi.
Phishing kiti indir SEO optimizasyonu, dijital pazarlama hedeflerimize ulaşmamıza yardımcı oldu. https://www.royalelektrik.com//istanbul-elektrikci/
Keep up the fantastic work!