Wachiwiri ku unduna owona za chilengedwe, Chipiliro Mpinganjira wati boma lipitilira kufalitsa ma uthenga a momwe anthu angapewere ngozi zogwa mwa dzidzidzi kaamba ka kusintha kwa nyengo ndicholinga chofuna kupulumutsa miyoyo ndi katundu ya anthu.
Ndunayi yanena izi lolemba mu m’zinda wa Lilongwe.
Iye wayamikila nthambi yoona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo kuti ikugwira ntchito yotamandika kamba kofalitsa ma uthenga a ngozi zogwa mwa dzidzidzi mu nthawi yoyenera.
” ineyo ndikuyamikila kwambiri ntchito yabwino imene anzathu a kunthambiyi akugwira. Ma uthenga akumapita patali ndipo akumayenda mwachangu. Ndipo anthu akudziwa kuti tikapitilira kuononga chilengedwe,tikapitilira kukhala m’malo osayenelera tipwetekeka ndife tomwe”, anatelo.
M’mawu mwake, mlembi wa bungwe la World Meteorological Organization, Celeste Saulo wayamikila boma la Malawi kuti likuchita bwino pofalitsa ma uthenga okhudza kupewa ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Iye wati ngakhale zili choncho, boma la Malawi likupitilira kukumana ndi mavuto a ngozizo choncho, likufunika thandizo kuti lizikhala lukonzekera pa mavut otelo.
Saulo wati bungwe lawo lithandiza dziko la Malawi kuti lizikonzekera ngozi zogwa mwadzidzidzi poonetsetsa kuti ma uthenga ochenjeza anthu ku ngozi zotelo akufikila wina aliyense komanso kulikonse.
Iye wati popita chitsogolo, bungwe lawo lipitilira kuthandiza boma kuti likhale patsogolo kusogoza nkhani za chilengedwe komanso kuteteza anthu amene ali pachiopsezo chokhuzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi.





















