Bwalo lamilandu (High Court) ku Phalombe lamasula bambo David Muthema litawapeza osalakwa pa mlandu wakupha.
Iwowa anawanga powaganizila kuti anadzetsa imfa ya Tambula Makwinja m’mwezi wa June 2015 zomwe ndizosemphana ndi gawo 209 lamalamulo aakulu adziko lino, Penal Code.
Pomwe Legal Aid Bureau imayendela kundende, idapeza iwowa ngati m’modzi mwa anthu ofunika nthandizo pa mlandu wawo chifukwa analibe owaimilira.
Mlandu wawo anawuyendetsa ndi Assistant Director Newton Mdazizira, Senior Legal Aid Advocate Martin Dallas komanso Senior Legal Aid Advocate Alfred Masamba.
Kubwalo lamilandu, ambali ya boma anabwera ndi mboni zinayi kuti zitsimikize ngati bamboyu analidi wolakwa.
Komabe woweluza mlanduwu, Justice Texious Masoamphambe, anapeza kuti mbali ya boma siinapereke umboni wokwanira kuti mpaka woganizilidwayu ayankhepo mlandu moikila umboni.
Bwalo lidapeza kuti panalibe mboni iliyonse yaboma yomwe inatsimikiza kuti David Muthema analidi munthu yemwe akuti anapalamula mlanduwo. Chomwe chinalipo ndi chikaiko chabe kuti mwina iyeyu anapalamuladi.
Bwaloli kotero lidalamula kuti bamboyu amasulidwe pamlandu wakupha.
Nkhaniyi yalembedwa ndi a Malawi Legal Aid Bureau