Anthu okhala mmudzi wa Chikho Mfumu yaikulu Kasakula m’boma la Ntchitsi ati ndi okondwa ndi ganizo la bungwe la WaterAid powabweretsa mjigo mu mudziwu.
Mfumu ya mmdziwu, Kalilani Tambala wati Kwa nthawi yaitali anthu akhala akusautsika ndi vuto la madzi ndipo amayenda mtunda wautali kukatunga madzi mu Phiri lomwe linazungulira mudziwu.
“amayi amayenda mtunda wautali kuzatunga madzi kuno ndipo zimatenganso nthawi yaitali kuti akafike ndi madziwo m’makwalala mwawo. Izi zimapangisaso kuti ana azichedwa kupita kusukulu Kamba koti madzi ali kutali”, anatelo Tambala.
Poonjezela, Tambala anati akhala akudandaula kwa nthawi yaitali kuti boma komanso mabungwe ena osiyanasiyana awathandize kuthana ndi vuto losowekela kwa madzi a ukhondo koma sizimaphula kanthu. Iye wati bungwe la WaterAid labwera munthawi yake kuzaombola anthu m’dera mwawo.
“M’mudzi mwanga muno tilibe mjigo olo ndi umodzi omwe kuyambira kalekale. Chitsime mukuchionachi chimamwetsa midzi isanunu ndi iwiri. Choncho ndife okondwa kuti a WaterAid atiganizila zedi kuti atibweretsele Mjigo kwathu kuno” Tambala anatelo.
M’mawu mwake,
Oyang’anila ntchito za ku ntchitsi ku bungwe la WaterAid, Laston Zungu wati madongosolo onse ali mkati kuti kontilakita ayambepo kukumba mjigo mu mudziwu.
Iye wati ndalama pafupifupi MK12 million kwacha ndizomwe zigwiritsidwe ntchito pokumba mjigowu.
“ Mjigo umenewu sukhala kutali ngati zakunoku koma tiuyandikisa kufupi ndi kumene kumakhala anthu kuti asamayende mtunda wautali” anatelo Zungu.