Bwalo lalikulu lamilandu m’boma la Nsanje lamasula mayi Fanlet Taulo Gideon ndi mayi Mwadaine Gideon omwe amaganizilidwa kuti anapha munthu mosemphana ndi gawo 208 la malamulo aakulu adziko lino – Penal Code.
Awiriwa amaganizilidwa kuti anadzetsa imfa ya Alick Gideon mwa chiwembu m’mwezi wa August 2018.
Amayiwa atamangidwa, anapempha thandizo la Legal Aid Bureau pomwe sanakwanitse kupeza loya womulipira. Atavomerezedwa kuti athandizidwa, anayimilidwa kubwalo la milandu ndi Assistant Director Sigele Beauty Chirwa komanso Senior Legal Aid Advocate Doreen Kawisa, mothandizidwa ndi Legal Aid Officer Effort Kusakala.
Kubwalo la milandu, amayiwa anapezeka kuti alibe mlandu wakuti ayankhepo chifukwa bwalo lidasonyeza kuti mbali ya boma siinapereke wina mwa umboni wofunikila. Mbali ya boma inakanika kutsimikiza kuti mchitidwe wa amayi awiriwa ndiwomwe unadzetsa imfa ya bambo Gideon.
Woweluza mlanduwu anatsimikiza kuti umboni wokwanira ulipo kuti bamboyu anafa, koma aboma sanafotokoze molunjika kuti kufa kwa munthuyu kunadza chifukwa cha mchitidwe wa amayi awiriwa.
Bwalo kotero lamasula amayiwa.
Nkhaniyi yachokela ku Legal Aid Advocate