Amene amafuna kupikisana nawo pa chisankho cha chipulula ku dera la kumpoto kwa kwa boma la Neno (Neno North Constituency), a Hebrews Misomali ati ndi okhumudwa ndi zimene chipani cha Democratic Progressive (DPP) chawachitira.
Malingana ndi a Misomali, ati chipanichi chinawakaniza kutenga mapepala owayeneleza kuti apikisane nawo pa zisankhozi kaamba kakuti ku delali kuli kale phungu wa DPP.
Phungu wa delali ndi a Thoko Tembo.
Iwo ati anauzidwa kuti ali ndi ufulu olowa zipani zina ngati anali osakhutitsidwa ndi ganizolo.
“Kuchokela tsiku Lomwe ine ndinakanizidwa ma pepala okapikisana nao ku ma primaries a DPP komanso kuuzidwa kuti ndikhoza ku joina zipani Zina poti kuno ku Neno North alipo kale MP, ndipomwe ndinadziwa kuti democracy ikukanika. Chipani sichimadzadza. Wawa angoni!
“Ku Mwanza ma MP ache anachotsedwa mu chipani, ku Neno South MP wache si wa DPP. Kunatsala ndi kuno ku Neno North. Kosonyeza kuti ngati uli genuinely wa ku Neno North chipani sichikutifuna. Kukondela Iwo okhao.
“Ndithokoze anthu omwe mukundiitana kuti ndikuyankhuleni pa zomwe zinachitikazi komanso Inu omwe mukuchoka mu chipanichi nkunditsata ine.
“Ine mdiima pa ndekha koma Inu omwe mumafuna kudzandivotela a chipani Cha DPP bwelani tikhale limodzi kuti tithetse khalidwe lomangovotela banja limodzi modzi Osatinso la kuno ngati ifeyo Eni ache ndife dzitsilu.
“Kaya ndinu a DPP, Kaya ndinu a zipani Zina kuno ku Neno North tiyeni tigwilane manja kuti chitukuko chibwele kunonso ku Neno North. Nafe tikhala ngati anzathu a kwaoko.
“Anthu awa akudziwa kuti ine ndikadzawina, ndidzafuna kuti ndalama zomwe boma limapeleka za CDF tidzazilindole kuti zagwila ntchito kuti. Nanga DDF yagwila ntchito kuti poti akuti kuno chitukuko sichibwela poti akuyendetsa boma si wa DPP chonsecho MP aliyense amalandila CDF yokwana 220million panopa, komanso district council iliyonse imalandila DDF ndiye kuno ku Neno zimagwila ntchito kuti?
“A MP athu sakhala kuno. Ma khansala onse nao samadziwa za CDF ndi DDF. Ngati amadziwa ndiye kuti amachita mwa dala kusowetsa ndalama za Chitukuko.
“Tilibe ma schools, zipatala, miseu yoonongeka simakonzedwa, tilibe nseu, mijigo ndinzina chonsecho ndalama boma limapeleka mosayangana nkhope.
“Ma boma onse amaoneka kuti safuna kulondola CDF ndi DDF kuti aone pomwe zagwila ntchito koma ulendo uno, tiyeni tigwila manja kuti tidziwe kuti ndalama zimenezi kuno ku Neno North zagwila pati ntchito.
“Ndithokoze anthu nonse omwe mukuchoka ku zipani Zina kuphatikiza DPP kundipatsa support kuti kuno tithane ndi umbava wa CDF komanso DDF kuti yemwe wasowetsa ndalamazi aimbidwe mulandu mopanda kukondela kapena kuti ifeyo tikamafunsa wina atiiopyeze ai.
“Ngati anthu simungafune ine, onetsetsani kuti pokavota osavotela anthu omwe aononga ndalama za chitukuko zaka 6 zapitazi MP ndi ma khansala ache.
“Ndithokoze olemekezeka a Muyatso pa boma ndi team yanu pondiitana komanso poonetsa chidwi chofuna kugwila ntchito ndi ine. Komanso ndithokoze nonse omwe munabwela pa nsonkhano umeneu kuchokela ma GVH osaiyana siyana. Chomwe Ife tikufuna ndi Chitukuko apo bi yemwe wadya ndalama za chitukuko ayambe kufuna ma lawyer Eni eni,” Iwo atelo kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Facebook