Katswiri wakale wa timu yachisodzera yadziko lino, Patrick Rudi wati zake zikuyenda bwino mulig yaying’ono ya mdziko la Mozambique.
Rudi anapita mdzikoli Chaka chatha, 2023 ku timu yotchedwa Ferrovuário de Moatize yomwe imasewela mu lig yomwe imapititsa ma timu mu lig yaikulu mdzikoli.
Chaka chake choyamba katswiriyu anakwanitsa kugoletsa zigoli zisanu ndichimodzi, ngakhale sanasewela masewero ambiri kamba kovulala.
Iye wati atabwelela chaka chino ku Mozambique, zinamutengela nthawi kuti ayambeso kusewela mpira kamba kakusamvana pakati pa timu yake ya Ferrovuário de Moatize komaso Teste de Phungwe yomwe inamupatsa kontalakiti.
“Chaka chino ndinakafikila ku Teste de Phungwe komwe ndinakayesa mwayi mpaka kupambana mayeso koma Ferrovuário de Moatize sinagwilizane ndi mtengo omwe ankafuna kundigulila ndipo zinakanika kusintha timu” anatero Rudi
Malingana ndi Rudi, chaka chino wasewela masewelo asanu ndi atatu (8) ndipo wakwanitsa kugoletsa zigoli zinayi mu lig komaso chimodzi mumpisano wina.
Kuchita bwino kwake kukupeleka chidwi kumatimu a lig yaikulu pomwe watitsimikizira kuti angapo afikila omuyimila kuti amutenge msika ukatsekulidwa.
Patrick Rudi anayambila mpira wake ku Silver Strikers yaying’ono mu 2016 komwe anasewela mpaka 2017.
Mu 2018 anayamba kusewela lig yaikulu mdziko muno ya TNM Super League ku timu ya Blue Eagles komweso anakhala zaka ziwiri mpaka 2019.
Muchaka cha 2020 anachita mgwirizano ndi Ekwendeni Hammers koma anayamba kusewela timuyi mu 2021 nthawi yomwe mipikisano inabwelelaso kutsatila tchuthi chachaka chimodzi kamba ka COVID.
Rudi anajoina Red Lions mu 2022 komwe anasewela chaka chimodzi kenaka ndipomwe amalowela ku Mozambique chaka cha 2023.
Katswiriyu anasewelaposo timu yadziko lino yachisodzera.