Sabata yakhumi mu TNM Super League yatha pomwe bungwe loyendetsa masewero mu mpikisanowu, la SULOM linachititsa masewero Lamulungu komaso lolemba lapitali.
Chidwi chinali pamasewero angapo kuphatikiza omwe FCB Nyasa Big Bullets imakumana ndi CRECK Sporting Club, Mighty Mukuru Wanderers yomwe imasewela ndi Civil Service United komaso Silver Strikers ndi Mighty Tigers.
Pamasewero omwe anali pa Civo Stadium pakati pa FCB Nyasa Big Bullets komaso CRECK Sporting Club Lamulungu lapitali, anawonetselatu kuti timu yawanthuyi ikudwala chaka chino.
Matimuwa atalephela kupeza chigoli muchigawo choyamba, Bullets inali yoyamba kugoletsa kudzela mwa Patrick Mwaungulu patatha mphindi 59, koma Gift Kadawati anachokela panja ndikukabweza patangotha mphindi zisanu ndiziwiri (7) kuti masewero athele 1-1.
Zotsatilazi zapangitsa kuti Bullets ikhalebe pa nambala yachisanu ndimapoint khumi ndi asanu (15) itasewela masewero khumi (10) ndipo ikuchepekedwa ndimapoint khumi ndi imodzi (11) kwaomwe akutsogola mumpikisanowu a Silver Strikers, yomwe ndimbiri yosakhala bwino ku Maule.
Chaka chatha, pamasewelo khumi Bullets inali itatolela mapoint 21 ndipo inkatsalira ndimapoint atatu okha kwa Silver Strikers yomwe inkatsogola.
Koma ngakhale sizikuyenda ku Bullets, Neba wawo Mighty Mukuru Wanderers akuwoneka kuti wagwila mseu tsopano kutsatila kukweza ntchito Meke Mwase yemwe analowa mmalo mwa Nsazurwimo Ramadhan amene nthawi yake ngati mphuzitsi wamkulu zinthu sizimayenda bwino.
Mwase anapeza Manoma atagonja kale kawiri komaso kufananitsa mphamvu katatu pamasewero asanu ndi atatu (8) ndipo inali pa nambala yachisanu koma katswiriyu wayipambanitsa Wanderers masewero onse awiri ndikuyitengela pa nambala yachitatu pomwe ili ndimapoint 18.
Atathandiza Manoma kutolela mapoint onse atatu pomwe anagonjetsa Dedza Dynamos 3-1 mmasewero ake oyamba, Meke Mwase anatamangitsaso Civil Service United yomwe anagonjetsa 3-0 kudzela muzigoli za Christopher Kumwembe kuti Nyerere zikhale ndichimwemwe chosefukila.
Karonga United inapambana masewero ake achitatu chiyambile mpikisano wachaka chino pomwe inagonjetsa Moyale Barracks 2-0.
Izi zikutanthauza kuti Ingwina tsopano ili pa nambala 11 ndimapoint ake 12 pomwe Moyale inaluza mwayi opita pa nambala yachinayi, kutsatila kugonjaku ili pa nambala 7 ndimapoint 14.
Chitipa United yomwe inamaliza pa nambala yachinayi chaka chatha, ikuvutika kwambiri chaka chino pomwe yakhazikika kuchigwa cha imfa pa nambala 14 kutsatilaso kugonja kwake itakumana ndi MAFCO lamulungu pa Chitowe.
Pakadali pano, Chitipa yangokwanitsa kupambana kamodzi kokha ndipo ili ndimapoint awiri mundandanda wamatimu amu TNM Super League.
Omwe anakumana nawo a MAFCO akuthawa chigwa cha imfa pang’ono ndi pang’ono pomwe zigoli ziwiri za Yohane Malunga ndi Peter Katsonga zinawathandiza kupambana ndikukwela kufika pa 12, mapoint awoso 12.
Bangwe All Stars ndi Mzuzu City Hammers anapata point imodzi aliyese atalephelana ndipo izi zapangitsa kuti akhalebe pomwe anali, Bangwe pa 14 ndimapoint 7 pomwe Hammers pa 4 mapoint ake 17.
Enanso omwe anagawana point imodzi-imodzi ndi FOMO komaso PremierBet Dedza Dynamos omwe analephelana 1-1, chigoli cha Arthur Kalondola ku FOMO FC yemwe anabweza kuchigoli ya Samson Olatubosun.
FOMO ili pa 13 ndima point 11 pomwe Dedza Dynamos ili pa 9 ndimapoint 12.
Atatha kugulugushana lamulungu, chidwi tsopano chinapita pabwalo la Kamuzu mumzinda wa Blantyre komwe otsogolela mpikisano wachaka chino Silver Strikers amakumana ndi eni bwalo Mighty Tigers.
Panali mwayi waukulu oti ma Banker akanawonjezela kusiyana kwawo ndiwachiwiri kufika pamapoint khumi (10) ngati Kamuzu Barracks ikanagonja ku Karonga.
Itangotaya mapoint awiri okha pamasewero asanu ndi anayi (9), lolemba lapitali linali tsiku lachiwiri chiyambile mpikisano wachaka chino kuti itaye mapoint ena.
Kawiri konse Messiah Kachingwe ndi Chimwemwe Ibrahim anabweza zigoli zomwe Silver Strikers imatsogola nazo kudzela mwa Duncan Nyoni komaso Nickson Mwase kuti masewelo athele 2-2.
Izi zinapangitsa Silver Strikers kuti idzitsogolabe ndimapoint asanu ndi awiri (7) pamwamba pa wachiwiri wake Kamuzu Barracks pomwe ili ndimapoint 26 pathodyo.
Ngakhale yayimitsidwa, zikuoneka kuti ma Banker awonjeza moto chaka chino kuposa chaka chatha pomwe anali ndimapoint 24 pamasewero khumi (10).
Ndipo kumbali ya Tigers, iyi inali point yoyamba kutenga pamasewero atatu ndipo inakwanitsa kuchoka pa 12 nkukakhala pa 10, mapoint ake 12.
Pomwe Silver Strikers imataya ma point ake awiri, nayoso Kamuzu Barracks yomwe ndiyachiwiri inachitaya pomwe inalephelana ndi Baka City posagoletsana chigoli chilichonse.
Asilikaliwa tsopano ali ndimapoint 19 pomwe Baka City yomwe sinapambanepo chiyambile mpikisano wachaka chino ili pansi penipeni ndimapoint anayi omwe yakwanitsa kutolela pongofanana mphamvu.
Your point of view caught my eye and was very interesting. Thanks. I have a question for you.