Mphuzitsi wamkulu wa Mighty Mukuru Wanderers Nsazurwimo Ramadhan watula pansi udindo wake.
Ramadhan watsanzika ku Wanderers kudzela mukalata yomwe walembela timuyi.
Izi zikutsatila kusachita bwino kwa timuyi pamasewero awiri omwe yasewera posachedwapa pomwe yagonja zigoli ziwiri kwa duuu mmanja mwa Silver Strikers komaso Mzuzu City Hammers.
Apa zikutanthauza kuti zomwe analonjeza Ramadhan kuti wabweletsa chimwemwe ku Wanderers zakanika pomwe wasiya timuyi itatsakamila panambala yachisanu (5) pamndandanda wamatimu a TNM Super League.
Atasewela masewero asanu ndiatatu (8), Manoma akwanitsa kutolela mapoint khumi ndi awiri (12), atapambana katatu, kufananitsa mphamvu katatu komaso kugonja kawiri.
Pakadali pano, timu ya Wanderers sinayankhulepo kanthu za nkhaniyi.