Monga mwa lamulo, Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lati lilimbe mphamvu iliyonse yosintha wapambuyo pa wopikisana pa udindo wa mtsogoleli wa dziko (running mate) pa zisankho zikubwelazi.
Mneneri wa bungweli Sangwani Mwafulirwa wanena izi lolemba paisankho
maphunziro a atolankhani mu m’zinda wa Lilongwe.
Iye wati bungwe lawo lilibe danga lililonse losinthila running mate wa chipani monga mwa lamulo.
Iye wati pa chisankho choyamba, lamulo m’dziko lino lidapeleka danga kuti running mate atha kusintidwa pokha- pokha ngati iye wamwalira, kapena ngati wavomeleza kuti sakufuna kupikisana nawo pa chisankho, ngatinso wapezeka kuti sali oyenela kupikisana nawo, komanso ngati wapezeka kuti ali osathekela kugwira ntchito.
Mwafulirwa anaonjezelanso kuti pa chisankho chachiwiri – chomwe ngati dziko lavota ndipo palibe mtsogoleri amene wapambana, amene wapeza mavoti osadutsila theka osachepela theka ya mavoti amene aponyedwa olungama (valid votes), iye wati lamulo limanena kuti pakhale chisankho cha anthu awiri amene apezeka pa nambala 1 ndi 2 ndipo ngati pangakhale kusintha kwa running mate zikhoza kuchitika ngati running mate wamwalira, akapezeka kuti samayenela kupikisana nawo pa chisankho, komanso akapezeka kuti sangathe kugwira ntchito.
Mwafulirwa wati izi ndizomwe ziyenela kusatidwa pofuna kusintha running mate.
























