Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati iye ndi okonzeka kuti atukwanidwe kutsatira mmene ngozi ya ndege imene anakwera wachiwiri wa dziko lino, Saulos Chilima.
Ndege yi inachita ngozi lolemba la sabata ino, pamene Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu anamwalira.
Poyankhula pa mwambo wa maliro wa Chilima ku bwalo la zamasewero la Bingu ku Lilongwe, Chakwera anavomeleza ponena kuti pa maliro aakulu ngati amenewa komanso imfa yadzidzidzi ngati imeneyi, zolakwilana sizilephera kukhalapo.
“Mukulira kwathu sitilephera kulakwilana mmaganizo, mmayankhulidwe, ndi mmachitidwe, koma chonde tiyeni tisazitengere ku mtima chifukwa izi zimachitika chifukwa chaululu omwe tikusowa nawo chochita.
“Olo ine ndemwe ndikudziwa kuti ino ndinthawi yoti ndivomeleze kutukwanidwa ndikunyozedwa chifukwa kholo lomwe likuyenera kuvomereza kulira kwa aliyense ndi ineyo, ndiye chonde sindikufuna kuti wina abwezere mzake zowawa chifukwa cha amene asankha kuti kulira kwawo aphatikizemo mau ondipezera ine zifukwa.
“Olira sitimawatseka pakamwa, chifukwa mukuliramo Mulungu amakhalanso akutitonthoza ndipo ife mbali yathu ikhalenso kutonthozana osati kubwezerana zowawa, chifukwa nkhondo siimanga mudzi.
“Ngati pali chinthu chimodzi chimene ndinaphunzira kwa Dr. Saulos Klaus Chilima muzaka zinayi mmene ndakhala ndikugwira naye ntchito ndiubwino okhala munthu oleza mtima, munthu okhala bwino ndi aliyense, munthu osatengera zolakwa za ena kumtima, munthu osasunga mangawa, munthu osanyanyalira dziko lake, komanso munthu opilira pa nthawi yomwe zinthu zasokonekela.
“Tataya munthu ofunikira kwambiri ndipo imfa imeneyi tiimva kuwawa nthawi yayitali, chifukwa ntchito zabwino zomwe apanga Dr. Saulos Klaus Chilima mdziko muno zakhuza anthu ambiri ndipo ndizosawerengeka. Ndiye pamene mitima yanu yasweka, Ambuye akufungatireni ndipo Mzimu Oyera akutonthozeni pamene tikumpempha Yesu kuti mzimu wa Saulos Chilima uuse mtendere,” anatelo Chakwera
Thupi la malemu Chilima liyikidwa mmanda mawa kumudzi kwawo, ku Nsipe, m’boma la Ntcheu.
Hello my loved one I want to say that this post is amazing great written and include almost all significant infos I would like to look extra posts like this