Mphekesera zikusonyeza kuti pali chikonzero chosintha bwalo lomwe lichititse masewero apakati pa Silver Strikers komaso Mighty Mukuru Wanderers.
Masewero a Super League-wa anayikidwa kuti achitike Lamulungu pa Silver Stadium koma malipoti akusonyeza kuti akhoza kuwapititsa pa bwalo Bingu.
Yemwe watitsina khutu wati izi zikubwela ngati njira imodzi yofuna kuthandiza masewero andime yotsiriza yampira wa akazi koma osewera ake atsikana omwe udzachitike pabwaloli pakati pa Ascent Academy komaso MDF Lioness kuti kudzakhale anthu ambiri.
Iye anatuso mbali zonse pakadali pano zagwilizana ndi ganizoli kupatula bungwe la Super League of Malawi.
“Pali ganizo loti masewero a Silver Strikers ndi Wanderers adzaseweredwe 5 koloko Lamulungu ikadzatha ndime yotsiliza ya mpira wa akazi”
“Monga mukudziwa Lamulungu kunaikidwa masewero onsewa nthawi yofanana ndipo kutha apo kudzakhalaso kunja kuliso masewero otsiliza a mpikisano waku England ndie izi zayika pachiwopsezo mpira watsikanawu kuti kutha kudzakhala anthu ochepa owonela”
“Koma pakadali pano nditha kukuuzani kuti zokambilana zakhala zili mkati ndipo ma timu a Silver Strikers ndi Wanderers komaso bungwe la FAM avomeleza ganizoli kwangotsala SULOM kuti inene mbali yake” iye anatero
Masiku apitawa, mmodzi oyankhulira nkhani zamasewero Joseph Kansampha anapempha bungwe la FAM kuti lisinthe masewero akazi andime yotsilizayi kuti kudzakhale anthu ambiri.
Mpikisano wa azimayiwu wakhala kuseweledwa koma awonela akhala asakulipila ndalama yapakhomo malingana ndichikonzero champikisanowu.