Mphunzitsi watimu ya Vanessa Sisters, Charles Brazio wati masomphenya ake ndiwotenga ukatswiri wa MPICO Netball League wachaka chino.
Brazio wayankhula izi patsogolo pamasewero awo oyamba omwe akukumana ndi Civonets mumpikisano wachaka chino wampira wamanja omwe amasewela ndi matimu atsikana achigawo chapakati.
Iye wati akulimba mtima kuti chaka chino ndichokolola kamba koti zokonzekera zawo zinayenda bwino.
“Zokonzekera zathu zayenda bwino, tagwiragwira malo onse pomwe mpikisano ukuyamba kumathero kwasabatayi”
“Atsikana anga ndiwokonzeka ndipo akufunitsitsa chikho chimenechi chitabwela ku Vanessa chaka chino”.
Atafunsidwa masomphenya ake chaka chino, Brazio anati; “Ifeyo kwakukulu tikufuna titakhala akatswiri a mpikisanowu koma ngati zingavute kwambiri, tikuyenela kuthela pachiwiri”.
Mphunzitsiyu wati ndiwokondwa kuti chaka chino akhala ndimpata osewela masewero ochuluka opimana mphamvu omwe akumulimbitsa mtima kuti achita bwino.
Vanessa Sisters inamaliza pa nambala yachisanu ndichinayi (9) chaka chatha zomwe Brazio wati zinali zosemphana ndikhumbo lawo.
Mpikisano wachaka chino wa MPICO ukuyamba loweluka likudzali koma Vanessa Sisters ikhala ndimasewero ake lamulungu pomwe idzakumane ndi Civonets.
Mpikisanowu umachitikira pabwalo lamasewero la Gateway Mall mumzinda wa Lilongwe.
Chaka chino kampani ya MPICO yomwe imathandiza mpikisanowu yawonjezera ndalama kuchoka pa K24 million kufika pa K40 million.