Yemwe adzaimile chipani cha Malawi Congress (MCP) ngati Phungu ku dera la Dedza Boma, Gerald Kampanikiza wayamikira anthu akufuna kwabwino a m’dera la a mfumu a Mkumkumbe kwa Mfumu Yayikulu Kamenyagwaza m’boma la Dedza kaamba komanga chipinda chomwe chili ndi ofesi ya mphunzitsi wamkulu, wachiwiri wake, aphunzitsi komanso Library pa sukulu ya pulayimale ya Msesa.
A Kampanikiza ayankhula izi pomwe anali mlendo pa mwambo opeleka chipindachi omwe wachitika pa sukulu ya Msesa Lachisanu masana.
Iwo ati zonyaditsa kuwona anthu omwe amachokera m’derali koma akukhala malo ena akukumbuka kwawo.
“Anthu ambiri amaiwala komwe akuchokera kotero zachitika lerozi zopatsa chidwi komanso zolimbikitsa angakhale kwa ine pa chidwi changa chofuna kusintha dera lino,” atero a Kampanikiza.
Ndipo pofuna kuwonetsa chidwi chawo pofuna kutukula maphunziro m’derali, a Kampanikiza alonjeza kuti agula mipando komanso madesiki omwe ayikidwe m’chipindachi.

Izi zakondweretsa Agulupu a Chimkombero omwe anaimira Mfumu Yayikulu Kamenyagwaza omwe ati anali ndi nkhawa yoti mipindo ichoka kuti koma zomwe alonjeza a Kampanikiza ndi chilimbikitso kuderali.
M’mau awo, a Damiano Samuel Gunde omwe ndi m’modzi mwa iwo omwe amanga chipindachi, apempha anthu pasukuluyi kuti asamale chipindachi ndi cholinga choti chipindulire anthu ochuluka.
“Tadzipeleka kuwonetsetsa kuti ana athu ndi aphunzitsi athu akhale ndi malo abwino zomwe zowapangitsa kukhala ndi chidwi cholimbikira komanso kukhala ndi chidwi pa maphunziro,” atero a Gunde.
Poyankhula, mlangizi wamkulu wa maphunziro a pulayimale m’boma la Dedza a Fredson Eric Njewa ati ngati unduna ngokondwa kaamba ka zomwe zachitikazi kaamba kakuti boma nthawi zonse limafuna anthu komanso mabungwe oti adzithandizana nawo potukula maphunziro.
Chipindachi chamangidwa ndi ndalama zokwana K15 million.